2 Samueli 14:32 - Buku Lopatulika32 Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa32 Abisalomu adayankha kuti, “Taona, ine ndinkatumiza mau kwa iwe kuti ndidzakutume kwa mfumu kukaifunsa kuti chifukwa chiyani ndidachoka ku Gesuri kubwera kuno? Kunali kwabwino koposa kuti ine ndizikhalabe konkuja.” Abisalomu adapitirira nati, “Ndipite basi kwa mfumu. Ngati ndili ndi cholakwa, mfumuyo ikandiphe.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’ ” Onani mutuwo |