Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 14:33 - Buku Lopatulika

33 Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Apo Yowabu adapita kwa mfumu, nakakambira mfumuyo zimenezo. Tsono mfumu idaitana Abisalomu. Iye adabwera kwa mfumu, nadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Ndipo mfumuyo idamlandira bwino pakumumpsompsona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anayiwuza zimenezi. Ndipo mfumu inamuyitanitsa Abisalomu, ndipo analowa nawerama kugunditsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. Tsono mfumu inapsompsona Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 14:33
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.


Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.


Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.


Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu aliyense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lake, namgwira, nampsompsona.


Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake.


Tsono mfumu Solomoni anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomoni; Solomoni nati kwa iye, Pita kwanu.


Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa