Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Zitapita zimenezi, Abisalomu adadzipezera galeta lokokedwa ndi akavalo, napezanso anthu makumi asanu omamperekeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Patapita nthawi, Abisalomu anadzipezera galeta ndi akavalo pamodzi ndi amuna makumi asanu amene amathamanga patsogolo pake.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:1
11 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.


Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni.


Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.


Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.


Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa.


Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.


Wokonda ndeu akonda kulakwa; ndipo wotalikitsa khomo lake afunafuna kuonongeka.


Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.


Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu aamuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa