2 Samueli 15:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima panjira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumzinda uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima pa njira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumudzi uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Abisalomu ankadzuka m'mamaŵa, namaima pa njira ya ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi mlandu kuti apite kwa mfumu kukaweruzidwa, Abisalomu ankamuitana, namufunsa kuti, “Ukuchokera ku mzinda uti?” Akayankha kuti, “Mtumiki wanune, ndine wa fuko lakutilakuti, m'dziko la Israele,” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Iye amadzuka mmamawa ndi kuyima pa njira yopita ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi zodandaula zopita nazo kwa mfumu kuti akaweruze, Abisalomu amamuyitana iye ndi kumufunsa kuti, “Kodi ukuchokera ku limodzi mwa mafuko a Israeli?” Onani mutuwo |