Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 15:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye amadzuka mmamawa ndi kuyima pa njira yopita ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi zodandaula zopita nazo kwa mfumu kuti akaweruze, Abisalomu amamuyitana iye ndi kumufunsa kuti, “Kodi ukuchokera ku limodzi mwa mafuko a Israeli?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima panjira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumzinda uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima pa njira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumudzi uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Abisalomu ankadzuka m'mamaŵa, namaima pa njira ya ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi mlandu kuti apite kwa mfumu kukaweruzidwa, Abisalomu ankamuitana, namufunsa kuti, “Ukuchokera ku mzinda uti?” Akayankha kuti, “Mtumiki wanune, ndine wa fuko lakutilakuti, m'dziko la Israele,”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:2
13 Mawu Ofanana  

Choncho Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita ku chipata cha mzinda wawo kukayankhula ndi anthu a mu mzindawo.


Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye. Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo.


Iwo anayankha kuti, “Ngati inu muwakomera mtima anthu awa ndi kuwasangalatsa ndiponso kuwayankha mawu abwino, iwo adzakutumikirani nthawi zonse.”


Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.


Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”


Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.”


Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha.


Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa; tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.


“Mʼmalo mwake mudzalowa munthu wonyozeka amene si wa banja laufumu. Iye adzabwera pamene anthu akuganiza kuti ali pa mtendere, ndipo adzalanda ufumuwo mwa chinyengo.


Mmamawa, akulu a ansembe onse ndi akuluakulu anavomerezana kuti aphe Yesu.


Ngati akubweretserani milandu mʼmabwalo anu imene ili yovuta kuweruza kaya ndi yokhetsa magazi, kaya ndi yophwanyirana ufulu, kaya ndi yovulazana, muyitengere kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.


Nthawi yomweyo Bowazi anapita ku chipata cha mzinda ndi kukhala pansi kumeneko pabwalo losonkhanira. Tsono anangoona wachibale woyenera kulowa chokolo uja akufika. Ndipo Bowazi anati, “Patukirani kuno, bwenzi langa. Mubwere mudzakhale apa.” Choncho anapatuka nakakhala pansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa