2 Samueli 22:23 - Buku Lopatulika Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga; ndipo za malemba ake, sindinawapatukire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga; ndipo za malemba ake, sindinawapatukira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Malamulo ake onse ali pamaso panga, sindinasiye malangizo ake. |
Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.
kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, mu ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele.
Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;
Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino;