2 Samueli 11:8 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire kunyumba yako, nutsuke mapazi ako. Ndipo Uriya anachoka kunyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire kunyumba yako, nutsuke mapazi ako. Ndipo Uriya anachoka kunyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Davide adauza Uriya kuti, “Pita kunyumba kwako, ukapumuleko.” Uriya adatuluka ku nyumba ya mfumu, ndipo mfumu idatumiza mphatso kukapereka kwa Uriya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya. |
Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.
Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya.
Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.
Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.
Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?
Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.
Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.
Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.