Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.
2 Samueli 1:12 - Buku Lopatulika Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo anthuwo adabuma maliro. Adalira ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Saulo ndi Yonatani mwana wake. Adaliranso chifukwa cha Aisraele, anthu a Chauta, chifukwa choti anali ataphedwa ku nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga. |
Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.
Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!
akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.
Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija.