Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 1:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndipo anthuwo adabuma maliro. Adalira ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Saulo ndi Yonatani mwana wake. Adaliranso chifukwa cha Aisraele, anthu a Chauta, chifukwa choti anali ataphedwa ku nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:12
10 Mawu Ofanana  

Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!”


Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako. Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.


Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi, ndi maso anga ngati kasupe wa misozi! Ndikanalira usana ndi usiku kulirira anthu anga amene aphedwa.


Mumamwera vinyo mʼzipanda zodzaza ndipo mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa Yosefe.


Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani


Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?


Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa.


Pambuyo pake anatenga mafupa awo ndi kuwakwirira pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.


Motero Sauli ndi ana ake atatu, wonyamula zida zake pamodzi ndi anthu ake onse anafera limodzi pa tsikulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa