2 Akorinto 7:9 - Buku Lopatulika Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kalikonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kalikonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma tsopano ndakondwa, osati chifukwa ndidaakupwetekani mtima, koma chifukwa kuvutika kwanu kudakuthandizani kutembenuka mtima. Kuvutika kwanuko kunali kovomerezeka ndi Mulungu, motero sitidakutayitseni kanthu kabwino kalikonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma tsopano ndine wokondwa, osati chifukwa chakuti kalatayo inakupwetekani, koma chifukwa chakuti chisoni chanu chinakuthandizani kutembenuka mtima. Pakuti munamva chisoni monga mmene Mulungu amafunira, choncho simunapwetekedwe mwanjira iliyonse. |
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.
Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.
Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.
ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata ija, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata ija inakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.