Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 15:7 - Buku Lopatulika

7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 15:7
13 Mawu Ofanana  

Pali mbadwo wodziyesa oyera, koma osasamba litsiro lao.


Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera.


Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:


Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.


Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwire lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatse ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.


Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.


Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nao, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.


Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza?


Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.


Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.


Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa