2 Akorinto 7:8 - Buku Lopatulika8 Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata ija, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata ija inakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Kalata yanga ija idakupwetekani mtima, komabe sindikuchita chisoni kuti ndidailemba. Ndidaachita chisoni poyamba, ndipo ndikuwona kuti kalatayo idakupwetekanidi mtima, ngakhale kanthaŵi pang'ono chabe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Ngakhale kalata yanga ija inakupwetekani mtima, sindikudandaula kuti ndinalemberanji. Ngakhale zinandikhudza, ndikudziwa kuti kalata yanga inakupwetekani, koma kwa kanthawi kochepa. Onani mutuwo |
Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.