2 Akorinto 4:11 - Buku Lopatulika Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti nthaŵi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake uwonekenso m'matupi athu amene amafa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa. |
Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.
Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha.
Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwa Khristu Yesu, Ambuye wathu.
nthawi zonse tilikusenzasenza m'thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu.
Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.
monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;