Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:31 - Buku Lopatulika

31 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwa Khristu Yesu, Ambuye wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwa Khristu Yesu, Ambuye wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Abale anga, imfa ndimayenda nayo tsiku ndi tsiku. Ndikunenetsa zimenezi chifukwa ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Abale, ndimafa tsiku ndi tsiku, ndikunenetsa zimenezi, mongotsimikizira monga ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:31
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.


Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawatulutsa iwo kudziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.


Ndipo mthenga wa Yehova anamchitira Yoswa umboni, ndi kuti,


koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'mizinda yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.


Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.


Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.


pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwake?


Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;


Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa