2 Akorinto 4:1 - Buku Lopatulika Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu mwa chifundo chake adatipatsa ntchitoyi, nchifukwa chake sititaya mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima. |
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.
Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.
Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.
amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.
Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;
Mwa ichi ndipempha kuti musade mtima m'zisautso zanga chifukwa cha inu, ndiwo ulemerero wanu.
ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;
Pakuti talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.
inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.