Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 7:25 - Buku Lopatulika

25 Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Kunena za amene sali pa banja, ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye. Koma ndikuuzani maganizo anga, ngati munthu amene Ambuye adandichitira chifundo kuti ndikhale wokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Tsopano za anamwali: Ine ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye, koma ndipereka maganizo anga monga ngati munthu amene mwachifundo cha Ambuye ndine wodalirika.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 7:25
15 Mawu Ofanana  

Moto unapsereza anyamata ao; ndi anamwali ao sanalemekezeke.


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.


Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,


Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.


Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.


Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.


Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.


Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira.


Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.


Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa