2 Akorinto 3:7 - Buku Lopatulika Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Malamulo ongolembedwa pa miyala aja adaperekedwa ndi ulemerero waukulu, kotero kuti Aisraele sankatha kuyang'anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha kuŵala kwake. Komabe kuŵala kwakeko kunali kosakhalitsa. Tsono ngati malamulowo, amene ali odzetsa imfa, adaperekedwa ndi ulemerero wotere, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala, |
Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.
Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.
Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa.
Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.
Pakuti Khristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa aliyense amene akhulupirira.
pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa.
Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;
Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso.
popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata ya Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.
amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.
Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi.
Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.
Pamenepo anakufotokozerani chipangano chake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.
Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?
Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.
Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a chipangano anali m'manja mwanga.
Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,
Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi.
okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;