2 Akorinto 3:3 - Buku Lopatulika3 popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata ya Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Anthu onse angathe kuwona kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, yolembedwa kudzera mwa ife, osati ndi inki koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa zolembapo zamiyala koma m'mitima mwa anthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu. Onani mutuwo |