Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:13 - Buku Lopatulika

13 Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Munatsikiranso pa phiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera m'Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mudatsika pa phiri la Sinai, ndipo mudalankhula nawo kuchokera kumwamba. Mudaŵapatsa malangizo olungama, malamulo oona, zophunzitsa zabwino ndiponso mau aluntha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “Munatsika pa Phiri la Sinai, ndipo munawayankhula kuchokera kumwamba. Munawapatsa malangizo olungama, ziphunzitso zoona ndiponso malamulo abwino.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:13
27 Mawu Ofanana  

ndi malemba, ndi maweruzo, ndi chilamulo, ndi choikika anakulemberani muzisamalira kuzichita masiku onse, nimusamaopa milungu ina;


Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.


Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.


Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.


Inu munatilamulira, tisamalire malangizo anu ndi changu.


Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.


Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.


Ndipo Mulungu ananena mau onse amenewa, nati,


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba.


Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu;


Pamene Inu munachita zinthu zoopsa, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu.


Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.


Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti chili chabwino.


Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala paphiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.


Kodi pali mtundu wa anthu udamva mau a mulungu wina akunena pakati pa moto, monga mudamva inu, ndi kukhala ndi moyo?


Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo padziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto.


Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?


Yehova ananena ndi inu popenyana maso m'phirimo, ali pakati pa moto,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa