Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:14 - Buku Lopatulika

14 ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mudaŵadziŵitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi lopatulika, ndipo mudaŵapatsa malamulo, malangizo, ndiponso mau anu, kudzera mwa Mose mtumiki wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Inu munawadziwitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi loyera ndipo munawapatsa malamulo ndi ziphunzitso.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:14
17 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.


Mukumbukire mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu;


Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;


Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.


Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.


Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.


Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Awa ndi malamulo, amene Yehova analamula Mose, awauze ana a Israele, m'phiri la Sinai.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israele, potuluka iwo mu Ejipito;


Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.


Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m'dziko limene ndiwapatsa likhale laolao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa