Ahebri 9:4 - Buku Lopatulika4 okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaphukayo, ndi magome a chipangano; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Chipindachi chinali ndi guwa lagolide lofukizirapo lubani. M'chipindamo munalinso bokosi lachipangano. Bokosi lonselo linali lokutidwa ndi golide. M'bokosimo munali kambiya kagolide m'mene munali mana uja, ndi ndodo ya Aroni, ija idaaphukayi. Munalinso miyala iŵiri ija yolembedwapo mau a chipangano. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano. Onani mutuwo |