Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Akorinto 2:7 - Buku Lopatulika

kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono makamaka nkwabwino mumkhululukire ndi kumlimbitsa mtima, kuwopa kuti angamve chisoni chachikulu chomtayitsa mtima kotheratu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mʼmalo mwake tsono, muyenera kumukhululukira ndi kumulimbikitsa mtima kuti asamve chisoni choposa muyeso, angataye mtima.

Onani mutuwo



2 Akorinto 2:7
20 Mawu Ofanana  

Akadatimeza amoyo, potipsera mtima wao.


Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa.


Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.


tiwameze ali ndi moyo ngati manda, ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;


Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.


Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.


Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.


Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.


Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.


Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.


Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.


kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;


Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.


Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.