Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,
2 Akorinto 10:7 - Buku Lopatulika Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ganizani bwino pa zimene mukuwona ndi maso anu. Kodi pali wina amene amakhulupirira kuti ndi wake wa Khristu? Chabwino, koma akumbukire kuti monga iye ali wake wa Khristu, ifenso ndife ake a Khristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mukuweruza potengera zimene maso anu akuona. Ngati wina akutsimikiza kuti ndi wake wa Khristu, iye aganizenso kuti ifenso ndife a Khristu monga iye. |
Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,
Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.
Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.
Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.
Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.
Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;
Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.
Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe.
Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.
popeza mufuna chitsimikizo, cha Khristu wakulankhula mwa ine; amene safooka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;
Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.
Ife ndife ochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife. Momwemo tizindikira mzimu wa choonadi, ndi mzimu wa chisokeretso.
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.