Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:23 - Buku Lopatulika

23 Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choundukula Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Koma aliyense adzauka pa nthaŵi yake: woyambirira ndi Khristu, ndipo pambuyo pake, pamene Khristuyo adzabwera, nawonso amene ali ake adzauka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:23
15 Mawu Ofanana  

Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.


Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.


kuti Khristu akamve zowawa, kuti Iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.


Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.


m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.


koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.


koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake.


Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.


Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.


Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.


ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.


Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwake?


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa