Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 5:12 - Buku Lopatulika

12 Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Sitikuyesa kudzichitiranso umboni pamaso panu ai, koma tingofuna kukupatsani chifukwa choti muzitinyadira. Tikufuna kuti mukhale ndi kanthu koŵayankha amene angonyadira zooneka ndi maso, osati zamumtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 5:12
13 Mawu Ofanana  

Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.


monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.


Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.


pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.


Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.


Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;


Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.


Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?


koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,


kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke mu Khristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa