2 Akorinto 1:23 - Buku Lopatulika Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu akhale mboni yanga, chifukwa chenicheni chimene sindidafikirenso ku Korinto chinali chakuti ndisakumvetseni chisoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni. |
Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu,
Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,
kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali mu Akaya monse:
koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi.
Choonadi cha Khristu chili mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya.
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.
Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;
m'mayeredwe, m'chidziwitso, m'chilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'chikondi chosanyenga;
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.
Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;
a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.