Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 4:21 - Buku Lopatulika

21 Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Nanga mukufuna chiyani? Mukufuna kuti ndidzabwere kwanuko ndi mkwapulo, kapena ndi mtima wachikondi ndi wofatsa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kodi musankha chiyani? Kodi ndidzabwere ndi chikwapu, kapena mu chikondi ndiponso mwa mzimu wofatsa?

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 4:21
16 Mawu Ofanana  

Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.


kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.


Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.


ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.


Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;


Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?


Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.


Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;


Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni.


Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse.


Pakutinso chimene chinachitidwa cha ulemerero sichinachitidwe cha ulemerero m'menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo.


Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.


Komatu tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ake a iye yekha;


Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa