Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.
1 Samueli 7:12 - Buku Lopatulika Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Samuele adatenga mwala, nauimiritsa pakati pa Mizipa ndi Sene, ndipo adautcha dzina loti Ebenezeri, ndiye kuti “Mwala wachithandizo,” pakuti adati, “Mpaka pano Chauta wakhala akutithandiza.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.” |
Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.
Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.
Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati padziko la Ejipito, ndi choimiritsa cha Yehova m'malire ake.
Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang'ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika;
amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;
Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.
Ndipo Saulo anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.
Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki.
Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.
Ndipo Aisraele anatuluka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betekara.