Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 4:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yoswa adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri imene idaali pakati pa mtsinje wa Yordani, pamalo pomwe padaaimirira ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja. Miyala imeneyi ikadali kumeneko mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yoswa anayimika miyala khumi ndi iwiri imene inali pakati pa Yorodani pamalo pamene ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anayimapo. Ndipo miyalayo ili pamalo pomwepo mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:9
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beereseba kufikira lero lino.


Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pamutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamutu pake.


ndi Abeeroti anathawira ku Gitaimu; kumeneko amakhalira kufikira lero lino.


Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.


Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.


Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.


Chifukwa chake munda umenewu anautcha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino.


Ndipo iwo analandira ndalamazo, nachita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.


Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino.


Ndipo Yoswa analembera mau awa m'buku la chilamulo cha Mulungu; natenga mwala waukulu, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pamalo opatulika a Yehova.


Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.


Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mzinda, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino.


Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ichi, chikhale lemba ndi chiweruzo pa Aisraele.


Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa