1 Samueli 4:21 - Buku Lopatulika Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mwanayo adamutchula dzina loti Ikabodi, ndiye kuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele!” Adatero chifukwa chakuti Bokosi lachipangano la Mulungu linali litalandidwa, ndiponso chifukwa cha imfa ya Eli mpongozi wake ndi ya mwamuna wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake. |
Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.
Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.
Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.
Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.
Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.
Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.