Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 3:12 - Buku Lopatulika

12 Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndidalankhula za Eli ndi banja lake, kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndinayankhula zokhudza banja la Eli kuyambira poyamba mpaka pomaliza.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 3:12
11 Mawu Ofanana  

ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupanga langa m'chimake, silidzabwereranso.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.


Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.


Ndipo dzanja la ana a Israele linankabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani.


Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.


Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa.


Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.


Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa