Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 78:61 - Buku Lopatulika

61 napereka mphamvu yake mu ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

61 napereka mphamvu yake m'ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

61 ndipo adalola adani athu kuti alande Bokosi la Chipangano chake, limene linali chizindikiro cha mphamvu zake ndi ulemerero wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

61 Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo, ulemerero wake mʼmanja mwa adani.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:61
10 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.


Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu; Inu ndi hema wa mphamvu yanu.


Weramutsani mitu yanu, zipata inu; ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.


Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera.


Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.


Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake aamuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.


Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa.


Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.


Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa