Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;
1 Samueli 2:28 - Buku Lopatulika Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo ndidamsankha pakati pa mafuko onse a Israele, kuti akhale wansembe wanga, ndipo kuti azipita ku guwa langa lansembe, azifukiza lubani, ndi kumavala efodi pamaso panga. Ndidalipatsa banja la bambo wako gawo la nsembe zanga zonse zopsereza zimene Aisraele amapereka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ndinamusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti akhale wansembe wanga ndi kuti azipita pa guwa langa la nsembe, kufukiza Lubani ndi kuvala efodi pamaso panga. Ndinapatsa banja la abambo ako gawo la nsembe zonse zopsereza zimene Aisraeli amapereka. |
Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;
Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.
Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.
Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m'mawa ndi m'mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize.
Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, achifukize chofukiza chosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu.
Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la chihema chokomanako achidye.
Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe ukhale nsembe yokweza yochokera ku nsembe zoyamika zanu.
limene Yehova analamula ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.
nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.
Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.
Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'chuuno ndi efodi wabafuta.