Eksodo 30:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m'mawa ndi m'mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m'mawa ndi m'mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 M'maŵa mulimonse Aroni azifukiza lubani wa fungo lokoma, ndipo nthaŵi yomweyo azikonza nyale zija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Aaroni ayenera kumafukiza lubani wonunkhira pa guwalo mmawa uliwonse. Pamene akukonza nyale zija afukizenso lubani. Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.