Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:36 - Buku Lopatulika

36 limene Yehova analamula ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 limene Yehova anauza ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Chauta ndiye amene adalamula Aisraele kuti azipereka zimenezi kwa ansembe, pa tsiku limene adadzozedwa. Zimenezo ndizo chigawo chao nthaŵi zonse pa mibadwo yao yonse.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Yehova ndiye analamulira kuti pa zopereka za Aisraeli azitapapo zimenezi ndi kuwapatsa ansembe ngati gawo lawo. Yehovayo analamula zimenezi pa tsiku limene ansembewo anapatulidwa ndipo anachikhazikitsa ngati lamulo la nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:36
6 Mawu Ofanana  

Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.


Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.


Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa