Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 6:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la chihema chokomanako achidye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la chihema chokomanako achidye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono Aroni ndi ana ake adye zimene zatsalapo. Zikhale zosafufumitsa, ndipo azidyere pa malo oyera, ndiye kuti pa bwalo la chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Aaroni ndi ana ake azidya zimene zatsala koma azidya zopanda yisiti ku malo wopatulika, ku bwalo la tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 6:16
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.


Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa.


Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.


Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.


Ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwira chimodzi cha izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo chotsalira chikhale cha wansembe, monga umo amachitira chopereka chaufacho.


Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya.


Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna, likhale lemba losatha.


chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa