Eksodo 28:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo zovala azisoka ndizi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Zovala zimene udzasokezo ndi izi: chovala chapachifuwa, chovala cha efodi, mkanjo, mwinjiro wopetedwa bwino, nduŵira ndi lamba. Asoke zovala zopatulikazo za mbale wako Aroni ndi za ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Zovala zoti apange ndi izi: chovala chapachifuwa, efodi, mkanjo, mwinjiro wolukidwa, nduwira ndi lamba. Apangire mʼbale wako Aaroni ndi ana ake aamuna zovala zopatulikazi kuti iwo anditumikire monga ansembe. Onani mutuwo |