Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 2:29 - Buku Lopatulika

29 Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Nanga chifukwa chiyani ukunyoza nsembe zanga ndi zopereka zanga zimene ndidalamula? Kodi ukulemekeza ana ako kupambana Ine, pomadzinenepetsa nonsenu ndi zakudya zokoma kwambiri za pa nsembe zanga zimene anthu anga Aisraele amapereka?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Nʼchifukwa chiyani ukunyoza nsembe ndi zopereka zanga zimene ndinalamula? Nʼchifukwa chiyani ukupereka ulemu kwa ana ako kuposa Ine podzinenepetsa nokha ndi zopereka zabwino kwambiri za nsembe zimene Aisraeli amapereka?’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:29
22 Mawu Ofanana  

Koma kunali, chaka cha makumi awiri mphambu zitatu cha mfumu Yowasi, ansembe sanathe kukonza mogamuka nyumba.


Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.


Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza.


Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga padzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.


Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?


Adyerera tchimo la anthu anga, nakhumbira chosalungama chao, yense ndi mtima wake.


Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.


Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;


Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.


Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.


Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.


amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.


Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.


Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa