1 Samueli 2:28 - Buku Lopatulika28 Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201428 Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa28 Ndipo ndidamsankha pakati pa mafuko onse a Israele, kuti akhale wansembe wanga, ndipo kuti azipita ku guwa langa lansembe, azifukiza lubani, ndi kumavala efodi pamaso panga. Ndidalipatsa banja la bambo wako gawo la nsembe zanga zonse zopsereza zimene Aisraele amapereka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero28 Ndipo ndinamusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti akhale wansembe wanga ndi kuti azipita pa guwa langa la nsembe, kufukiza Lubani ndi kuvala efodi pamaso panga. Ndinapatsa banja la abambo ako gawo la nsembe zonse zopsereza zimene Aisraeli amapereka. Onani mutuwo |