Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 12:5 - Buku Lopatulika

Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wake ali mboni lero kuti simunapeze kanthu m'dzanja langa. Nati iwo, Iye ali mboni.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wake ali mboni lero kuti simunapeza kanthu m'dzanja langa. Nati iwo, Iye ali mboni.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo Samuele adaŵauza kuti, “Chauta ndiye mboni pakati pa ine ndi inu, nayenso wodzozedwa wa Chauta ndiye mboni lero lino kuti simudandipeze chifukwa chilichonse.” Ndipo iwo adati, “Zoonadi, Chauta ndiye mboni.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.” Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.”

Onani mutuwo



1 Samueli 12:5
14 Mawu Ofanana  

Ukasautsa ana anga aakazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako.


Tsopanonso, taona, mboni yanga ili kumwamba, ndi nkhoswe yanga ikhala m'mwamba.


Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.


Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.


Akachipeza chakubacho chili m'dzanja lake chamoyo, ngakhale ng'ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.


Pilato ananena kwa Iye, Choonadi nchiyani? Ndipo pamene adanena ichi, anatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, Ine sindipeza konse chifukwa mwa Iye.


Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye?


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza chosalungama chotani, poimirira ine pamaso pabwalo la akulu a milandu,


Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Ndipo iwo anati, Simunatinyenge, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina aliyense.


Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?