Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 18:38 - Buku Lopatulika

38 Pilato ananena kwa Iye, Choonadi nchiyani? Ndipo pamene adanena ichi, anatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, Ine sindipeza konse chifukwa mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Pilato ananena kwa Iye, Choonadi nchiyani? Ndipo pamene adanena ichi, anatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, Ine sindipeza konse chifukwa mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Pilato adamufunsa kuti, “Choona nchiyaninso?” Pilato atanena mau ameneŵa, adatulukiranso kwa Ayuda, naŵauza kuti, “Ine munthuyu sindikumpeza chifukwa chilichonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Pilato anafunsa kuti, “Kodi choonadi nʼchiyani?” Ndi mawu awa iye anapitanso kwa Ayuda ndipo anati, “Ine sindikupeza mlandu mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 18:38
14 Mawu Ofanana  

Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.


Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsatu, Mpachikeni Iye.


Ndipo Pilato anati kwa ansembe aakulu ndi makamu a anthu, Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.


Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?


Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse.


Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.


Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.


koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa