1 Samueli 26:9 - Buku Lopatulika9 Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Koma Davide adamuuza kuti, “Ai, usamuphe. Ndani angathe kupweteka wodzozedwa wa Chauta nakhala wosachimwa?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Koma Davide anamuyankha Abisai kuti, “Usamuphe! Ndani adzapha wodzozedwa wa Yehova ndi kupezeka wosalakwa? Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.