Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 24:16 - Buku Lopatulika

16 M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nchifukwa chake inenso ndimayesetsa nthaŵi zonse kukhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu, ndi pamaso pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Kotero ine ndimayesetsa kuti ndikhale ndi chikumbumtima chosanditsutsa pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 24:16
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.


popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbumtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana;


Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,


Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu;


Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


ndi kukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chao chidatayika;


koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;


okhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m'chikumbu mtima choona.


Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,


Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.


koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.


ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.


chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa