Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.
1 Samueli 1:20 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “Ndidachita kumpempha kwa Chauta.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.” |
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.
Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwake.
Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha.
namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pantchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;
Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.
Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.
Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;