Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 1:18 - Buku Lopatulika

Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Chomwecho mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Chomwecho mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Hana adati, “Mundikomerebe mtima mdzakazi wanune.” Pompo mkaziyo adachoka nakadya, ndipo sadaonekenso wachisoni.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hana anati, “Mundikomerebe mtima mtumiki wanune.” Kenaka anachoka nakadya, ndipo sanaonekenso wachisoni.

Onani mutuwo



1 Samueli 1:18
11 Mawu Ofanana  

ndipo ndili nazo ng'ombe ndi abulu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako.


Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.


Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.


Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.


Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.


Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.


Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.


Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.