Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 33:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Apo Esau adati, “Tsono undilole kuti ndikusiyire anthu anga enaŵa.” Koma Yakobe adati, “Iyai mbuyanga, zimenezo sizifunika kwenikweni, ndingofuna kukukondwetsani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Esau anati, “Ndiye bwanji ndikusiyireko ena mwa anthu anga.” Koma Yakobo anati, “Koma muchitiranji zimenezi? Chachikulu nʼkuti mwandilandira bwino, mbuye wanga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 33:15
8 Mawu Ofanana  

Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.


Ndipo Esau anabwerera tsiku lomwelo kunka ku Seiri.


Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.


Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.


Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.


Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.


Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Chomwecho mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.


Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; chifukwa chake muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tilikufika tsiku labwino; mupatse chilichonse muli nacho m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa