Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 2:2 - Buku Lopatulika

2 Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsiku lina Rute adauza Naomi kuti, “Mundilole kuti ndikakunkhe barele ku munda wa munthu aliyense amene akandikomere mtima.” Naomi adamuuza kuti, “Pita mwana wanga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsiku lina Rute, Mmowabu uja anati kwa Naomi, “Mundilole kuti ndikakunkhe barele ku munda wa munthu aliyense amene akandikomere mtima.” Naomi anati kwa iye, “Pita mwana wanga.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:2
9 Mawu Ofanana  

Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.


Usamakunkha khunkha la m'munda wako wampesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wampesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.


Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.


Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.


Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.


ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.


Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Chomwecho mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa