Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 2:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Naomi anali naye mbale wa mwamuna wake, ndiye munthu mwini chuma chambiri wa banja la Elimeleki; dzina lake ndiye Bowazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Naomi anali naye mbale wa mwamuna wake, ndiye munthu mwini chuma chambiri wa banja la Elimeleki; dzina lake ndiye Bowazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Naomi anali ndi wachibale wake wachuma kwambiri, wa m'banja la malemu mwamuna wake uja Elimeleki, dzina lake Bowazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Naomi anali ndi mʼbale wake wolemera kwambiri wochokera ku banja la mwamuna wake Elimeleki, dzina lake Bowazi.

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:1
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israele ndalamazi, nasonkhetsa achuma, yense masekeli makumi asanu a siliva, kuti azipereke kwa mfumu ya Asiriya. Nabwerera mfumu ya Asiriya osakhala m'dzikomo.


Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.


ngati ndinakondwera popeza chuma changa nchachikulu, ndi dzanja langa lapeza zochuluka;


ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese;


mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Nasoni,


Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.


Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.


Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera cholowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.


Nanga Bowazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ake? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.


ndi Salimoni anabala Bowazi, ndi Bowazi anabala Obedi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa