1 Akorinto 4:4 - Buku Lopatulika Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndilibe kanthu konditsutsa mumtima mwanga, komabe ngakhale chimenechi si chitsimikizo chakuti ndine wolungama. Ondiweruza ndi Ambuye basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, koma sikuti ndine wolungama. Wondiweruza ine ndi Ambuye. |
Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
Chinkana ndikhala wolungama, pakamwa panga padzanditsutsa; chinkana ndikhala wangwiro, padzanditsutsa wamphulupulu.
Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.
Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.
Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu; koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova.
Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.
Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.
pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.
Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai.
Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.