Machitidwe a Atumwi 23:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbu mtima chokoma chonse kufikira lero lomwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Paulo adaŵapenyetsetsa a m'Bwalo Lalikulu aja nati, “Abale anga, ine moyo wanga wonse mpaka lero lino ndakhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Paulo anayangʼanitsitsa anthu a Bwalo Lalikulu nati, “Abale anga, ndakhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu mpaka lero lino.” Onani mutuwo |